Back to News March 25, 2026 news

Chipata cha Ngolongoliwa chipitilira kumangidwa posachedwa

Phungu wa dera la Thyolo-Goliati olemekezeka a Maureen Namwali asindika kuti ntchito yomanga chipatala cha Ngolongoliwa yomwe idaima m'chaka cha 2020 ikuyembekezereka kuyambaso kusatira kuvomelezedwa kwa ndondomeko ya chuma cha boma ya 2026 mpaka 2027. A Namwali ati ichi chidali chikonzero chawo mogwilizana ndi anthu adera lawo kuti kupitilira kumangidwa kwa Chipatala cha Ngolongoliwa chizakhare patsogolo chifukwa ntchito idaima m'chaka cha 2020 kuchokera m'chaka cha 2017 pomwe idayambika. "Mumkumano wa aphungu nyumba ya malamulo pa 16 March 2026 ndidakumbutsa nduna ya zaumoyo olemrkeza a Madalitso Boyidi zakufunika kwakumaliza kumanga chipatalachi pofuna kupititsa patsogolo umoyo wabwino kwa anthu ozungulira malo omwe ku kumangidwa chipatala cha Ngolongoliwa chomwe chili m'dera langa la Thyolo-Goliati ". A Namwali kufotokoza. Kupatula kuti chipatala cha Ngolongoliwa chipitilira kumangidwa Phunguyu wayamikira zakuvolemezedwa kwa ndondomekoyi lachiwiri pa 24 March 2026 motsogozedwa ndi nduna ya zachuma a Joseph Mwanamvekha pansi pa boma la DPP, ndondomekoyi ithandizira mma gawo a za ulimi, maphunziro ndiso zitukuko zosiyanasiyana.