Back to News March 25, 2026 news

Amene amapapemphera ndi amene amapambana mchifukwa chake ine Phungu wa dera la Thyolo-Goliati ndakonza mapemphero a Mayi pa 27 March 2026.

Phungu wa dera la Thyolo-Goliati Maureen Namwali wati kukondeledwa komwe Mulungu amamuonesera ndikomwe kumapasa nyonga zotumikira mwatotomoyo anthu a m'dera lake mchifukwa akuchititsa mwambo wa mapemphero lachisanu pa 27 March 2026 pa bwalo la masewero la sukulu ya sekondale yoyendera ya Matapwata m'boma la Thyolo. Malinga ndi Phunguyu mapempherowa ndi amayi onse amdera la Thyolo-Goliati posayang'anira chipembezo chawo ndipo iye wapitilira kuitana Amayi omwe siokhawo adera la Thyolo-Goliati kuti azafike ku mwambowu omwe uzayambe 8koloko m'mawa. Kupatula mapemphero ku mwambowu kuzakharaso maimbidwe kuchokera ku magulu osiyanasiyana a mma tchalitchi onse omwe azabwere ndipo Daughter of Zion ndi oimba wamkulu yemwe azapezeke ku mwambowu ndikusisimusa amayi ndi nyimbo za uzimu.