Back to News
March 20, 2026
news
Ndikukufunirani inu ndi banja lanu, Eid yodzaza ndi chimwemwe, mtendere ndi madalitso ochuluka.
Phungu wa nyumba ya malamulo kudera la Thyolo-Goliati Maureen Namwali wafunira zabwino asilamu mdziko muno pomwe akuchita chikondwelero cha mwambo wa Eid Mubarak kusatira kuoneka kwa mwezi lachisanu pa 20 March 2026 ndipo mapemphero a Eid Ul Fitr achitika loweraka pa 21 March 2026.
"Allah akulandireni mapemphero anu onse, akukhululukireni machimo anu, ndiponso akudalitseni pa moyo wanu wonse." watero Namwali
Phunguyi walimbikitsa chikondi, kuthandizana, ndi kugawana chimwemwechi ndi ena, makamaka omwe ali osowa.