Back to News
May 2, 2026
news
Kulimbikira ntchito ndilofunika pachitukuko cha anthu mdziko muno.
Phungu wa dera la Thyolo-Goliati Olemekezeka Maureen Namwali walimbikitsa mzika za dziko lino kuchilimika pogwira ntchito pofuna kuthana ndi umphawi ndiso kutukula dzikoli.
A Namwali ayankhula izi pa 1 May 2026 lomwe ndi tsiku la lokumbukira anthu apa ntchito zosiyanasiyana.
"Ndikufinira tsiku labwino latchuti kwa onse apa ntchito kuti kudzera mu ntchito yomwe amagwira ipundulire iwo komaso dziko lino." watero phunguyu mu uthenga wake wapadera.