Back to News
May 2, 2026
news
Mulungu adasankha A Dad kuti azaombore dziko lino.
Phungu wa dera la Thyolo-Goliati Olemekezeka Maureen Namwali wati utsogoleri wa chipani cha DPP motsogozedwa ndi mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika adasankha ndi Mulungu kudzera mwa anthu omwe amazuzinka mdziko lino.
A Namwali adayankhura izi pomwe mtsogoleri wa dziko linoyu adayendera anthu a kwa Goliati pambuyo pozara Nkhata pa manda a mchimwene wawo yemweso ndi mtsogoleri wachitatu wa dziko lino malemu Dr Bingu Wa Mutharika.
Phunguyu wati mu miyezi yochepa yomwe boma la DPP lidatenga boma umoyo wa anthu wasintha m'magawo onse zomwe ndi umboni oti utsogoleri ulipowu ndi odalitsidwa.